Jeremiah 32:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikuru ndi mkono wanu wotambasuka; palibe cokulakani Inu;