Jeremiah 32:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zolinga zanu nzazikulu, ndipo ntchito zanu nzamphamvu. Maso anu amaona makhalidwe onse a anthu. Ndipo aliyense mumampatsa mphotho malinga ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wamkulu m'upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu. Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita. Mumapereka mphotho kwa munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
wamkuru, m'upo, wamphamvu m'nchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa cipatso ca macitidwe ace;