Jeremiah 32:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mudachita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa ku Ejipito, ndipo mwakhala mukuzichitabe mpaka pano, pakati pa Israele ndiponso pakati pa anthu onse. Motero mwatchukitsa dzina lanu mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, m'Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ku Igupto, ndipo mwakhala mukuzichita mpaka lero, pakati pa Aisraeli ndiponso pakati pa anthu onse. Choncho mwadzitchukitsa mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, m'Israyeli ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;