Jeremiah 32:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaloŵa nkulilanda kuti likhale lao. Koma iwo sadakumvereni, sadatsate malamulo anu. Sankachita zimene mudaaŵalamula. Nchifukwa chake mwaŵagwetsera mavuto onseŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analowa nʼkulitenga kukhala lawo, koma sanamvere Inu kapena kutsatira lamulo lanu; ndipo sanachite zomwe munawalamula. Choncho inu mwawagwetsera masautso onsewa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo analowa, nakhalamo; koma sa namvera mau anu, sanayenda m'cilamulo canu; sanacita kanthu ka zonse zimene munawauza acite; cifukwa cace mwafikitsa pa iwo coipa conseci;