Jeremiah 32:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani, adani akuzinga ndi nthumbira zankhondo mzindawu kuti aulande. Mzinda umenewu udzaperekedwa kwa Ababiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi, monga mwadziwonera nokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha chaola; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Onani momwe adani azingira ndi mitumbira yankhondo mzindawu kuti awulande ndipo akuwuthira nkhondo. Chifukwa cha lupanga, njala ndi mliri. Mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni anthu atafowoka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi monga mukuzionera tsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la, Akasidi olimbana nao, cifukwa ca lupanga, ndi cifukwa ca njala, ndi cifukwa ca caola; ndipo cimene munacinena caoneka; ndipo, taonani, muciona.