Jeremiah 32:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababiloni, Inu Chauta mudandilamula kuti ndigule mundawo pali mboni ziŵiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Ababiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni, komabe Inu Ambuye Yehova, munandiwuza kuti, ‘Gula munda ndi siliva ndipo upereke ndalamazo pali mboni.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Akasidi.