Jeremiah 32:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo Ababiloni amene akuuthira nkhondo, adzaloŵamo. Adzautentha ndi kugwetsa makamaka nyumba zimene padenga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukizapo lubani kwa Baala ndi poperekapo chopereka cha chakumwa kwa milungu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Ababiloni, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Ababuloni amene akuwuthira nkhondo mzinda uno adzalowa ndi kuwutentha; adzatentha ndi kugwetsa nyumba zimene pa denga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukiza lubani kwa Baala ndi popereka chopereka cha chakumwa kwa milungu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Akasidi, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa macitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu yina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.