Jeremiah 32:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zedekiya mfumu ya ku Yuda ndiye amene adaamtsekera m'menemo. Mfumuyo idaamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani iwe ukulosa zakuti, Chauta akunena kuti, ‘Mzindawu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Zedekiya mfumu ya Yuda nʼkuti itamutsekera mʼmenemo, ndipo inati, “Nʼchifukwa chiyani ukulosera motero? Iwe ukunena kuti, ‘Yehova akuti: Ndidzapereka mzinda uno kwa mfumu ya ku Babuloni, ndipo idzawulanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Cifukwa canji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo iye adzaulanda,