Jeremiah 32:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiyambire pa ubwana wao, Aisraele ndi Ayuda akhala akungochita zoipa pamaso panga, nkumandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aisraeli ndi Ayuda akhala akuchita zoyipa zokhazokha pamaso panga kuyambira ubwana wawo. Kunena zoona Aisraeli akumandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa, akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Yuda anacita zoipa zokha zokha pamaso panga ciyambire ubwana wao, pakuti ana a Israyeli anandiputa Ine kokha kokha ndi nchito ya manja ao, ati Yehova.