Jeremiah 32:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala m'chigwa cha Benihinomu, kuti apereke ana ao aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Sindidalamule zimenezo ndine, ndipo sindidaganizeko kuti iwo nkuchita zonyansa zoterezi, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda pakutero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinauza, chimene sichinalowa m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamanga malo opembedzerapo Baala mʼChigwa cha Hinomu kuti aziperekapo ana awo aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Ine sindinawalamulire kutero, ndipo sindinaganizepo nʼkomwe kuti iwo angachite chinthu chonyansa chotero, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamanga misanje ya Baala, iri m'cigwaca mwana wace wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao amuna ndi akazi cifukwa ca Moleki; cimene sindinauza, cimene sicinalowa m'mtima mwanga, kuti acite conyansa ici, cocimwitsa Yuda.