Jeremiah 32:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ponena za mzinda umenewu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Komatu zimene Chauta, Mulungu wa Israele akunena ndi izi:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu ponena za mzindawu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni mwa nkhondo, njala ndi mliri, koma Yehova Mulungu wa Israeli akuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babulo ndi lupanga, ndi njala, ndi caola: