Jeremiah 32:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuti, “Ine ndidzaŵasonkhanitsa anthuŵa kuchokera ku maiko onse kumene ndidaŵapirikitsira ndili wokwiya, waukali ndi wopsa mtima kwambiri. Ndidzaŵabwezanso ku malo ano, ndipo adzakhala kuno ndi mtendere wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzawasonkhanitsadi anthuwa kuchokera ku mayiko onse kumene ndinawapirikitsira ndili wokwiya ndi waukali kwambiri. Ndidzabwera nawo ku malo ano ndipo ndidzawalola kukhala mwamtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapitikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukuru, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,