Jeremiah 32:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zedekiya mfumu ya ku Yuda sadzapulumuka kwa Ababiloni, koma adzaperekedwa ndithu kwa mfumu ya ku Babiloni. Adzaonana naye maso ndi maso nadzalankhula naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zedekiya mfumu ya Yuda sidzapulumuka mʼmanja mwa Ababuloni, koma idzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni. Adzayankhula naye ndi kuonana naye maso ndi maso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Akasidi, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;