Jeremiah 32:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adzaguladi minda ndi ndalama. Mapangano ake adzalembedwa, adzamatidwa ndipo padzakhala umboni wake ku dera la Benjamini, ku malo oyandikana ndi Yerusalemu, m'mizinda ya ku Yuda, m'mizinda yakumapiri, m'mizinda yakuchigwa ndi yakumwera ku Negebu. Zoona, ndidzaŵabwezera ufulu wao,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kuchidikha, ndi m'midzi ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzagula minda ndi ndalama zasiliva, ndipo achita pangano, ndi kumata pamaso pa mboni. Izi zidzachitika mʼdziko la Benjamini, ku malo ozungulira Yerusalemu, mʼmizinda ya Yuda, mʼmizinda ya ku mapiri, mʼmizinda ya kuchigwa ndi yakummwera ku Negevi. Zoona, ndidzabwezera ufulu wawo, akutero Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kucidikha, ndi m'midzi ya ku Mwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.