Jeremiah 32:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zedekiya adzatengedwa kupita ku Babiloni, ndipo adzakhala kumeneko mpaka nditamkhaulitsa, akutero Chauta. Ngakhale iye adzamenyane nawo chotani Ababiloniwo, sadzatha kuŵapambana.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zedekiya adzatengedwa kupita naye ku Babuloni, kumene adzakhale mpaka nditamukhawulitsa, akutero Yehova. Ngakhale iye adzamenyane ndi Babuloni, koma sadzapambana.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babulo, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Akasidi, simudzapindula konse?