Jeremiah 32:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe Chauta adanenera, Hanamele msuweni wanga adadzandiwonadi ku bwalo la alonda. Iyeyo adati, ‘Gula munda wanga ku Anatoti m'dziko la Benjamini, poti iwe ndiye woyenera kuuwombola kuti ukhale choloŵa chako.’ Tsono ndidadziŵa kuti umenewu unali uthenga wa Chauta uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo monga momwe Yehova ananenera, Hanameli, msuweni wanga anabweradi ku bwalo la alonda ndipo anati, “Gula munda wanga wa ku Anatoti mʼdziko la Benjamini. Popeza ndiwe woyenera kuwugula ndi kukhala wako, gula munda umenewu kuti ukhale wako.” “Ine ndinadziwa kuti amenewa anali mawu a Yehova aja;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.