Jeremiah 33:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mau achisangalalo ndi achimwemwe, mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. M'Nyumba ya Mulungunso mudzamveka nyimbo ya anthu odzapereka nsembe zothokozera Mulungu. Nyimbo yake azidzati, “ ‘Tamandani Chauta Wamphamvuzonse, popeza kuti ndi wabwino ndipo chikondi chake nchamuyaya!’ Ndithudi, ndidzaŵabwezeranso pabwino monga momwe adaaliri,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mfuwu wachimwemwe ndi mawu achisangalalo, mawu a mkwatibwi ndi mkwati. Mʼnyumba ya Mulungu mudzamvekanso nyimbo za anthu amene akudzapereka nsembe zothokoza Yehova. Azidzati, “Yamikani Yehova Wamphamvuzonse, popeza Iye ndi wabwino; pakuti chifundo chake nʼchamuyaya.” Pakuti ndidzabwezeretsa zinthu zabwino za dziko lino monga zinalili poyamba, akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, cifundo cace ncosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.