Jeremiah 33:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku mizinda yakumapiri, ku chigwa, kumwera ku Negebu, ku dera la Benjamini, ku maiko oyandikana ndi Yerusalemu ndiponso ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzapitanso pamaso pa munthu woziŵerenga,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'midzi ya kumtunda, m'midzi ya kuchidikha, m'midzi ya kumwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'midzi ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku mizinda ya kumapiri, ya kuchigwa, ya ku Negevi, ya ku dera la Benjamini, ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzadutsanso pamaso pa munthu woziwerenga,’ akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'midzi ya kumtunda, m'midzi ya kucidikha, m'midzi ya ku Mwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'midzi ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.