Jeremiah 33:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo ndiponso pa nthaŵi yomweyo, ndidzaphukitsa nthambi yolungama kuchokera kubanja kwa Davide. Munthuyo adzachita zabwino ndi zolungama m'dziko lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dzikomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mʼmasiku amenewo ndi pa nthawi imeneyo ndidzaphukitsa Nthambi yolungama kuchokera ku banja la Davide; munthuyo adzachita zolungama ndi zabwino mʼdziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukitsira Davide mphukira ya cilungamo; ndipo adzacita ciweruzo ndi cilungamo m'dzikomu.