Jeremiah 33:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo anthu a ku Yuda adzapulumuka, ndipo a ku Yerusalemu adzakhala pa mtendere. Motero mzindawu udzakhala ndi dzina loti ‘Chauta ndiye chipulumutso chathu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumuka ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere. Dzina limene mzindawu udzadziwike nalo ndi ili: Yehova Chilungamo Chathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzachedwa nalo, Yehova ndiye cilungamo cathu.