Jeremiah 33:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzimodzinso ndidachita chipangano ndi Davide, mtumiki wanga, kuti nthaŵi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndidachitanso chipangano china ndi ansembe Achilevi kuti iwowo adzanditumikira nthaŵi zonse. Ndipo zipangano zimenezi sizingaphwanyike konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinachitanso pangano ndi Davide, mtumiki wanga kuti nthawi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndinachitanso pangano ndi Alevi kuti iwonso adzanditumikira nthawi zonse. Mapangano amenewa sadzaphwanyidwa nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wace; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.