Jeremiah 33:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachulukitsa zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndi atumiki anga ansembe Achilevi, kuchuluka kwake ngati kwa nyenyezi zakuthambo kapena kwa mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachulukitsa ngati nyenyezi zamlengalenga ndiponso ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndiponso za Alevi amene amanditumikira Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mcenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; comweco ndidzacurukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.