Jeremiah 33:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono monga ndachita zimenezi motsimikiza, chonchonso ndidzachisunga chipangano chimene ndidachita ndi zidzukulu za Yakobe, ndiponso ndi Davide, mtumiki wanga. Ndidzasankhula mmodzi mwa zidzukulu za Davide kuti azilamulira zidzukulu za Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Komatu tsono ndidzaŵamvera chifundo ndi kuŵabwezeranso pabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
monga ndachita zimenezi motsimikiza, choncho ndidzasunga pangano limene ndinachita ndi zidzukulu za Yakobo ndi Davide mtumiki wanga. Ndidzasankha mmodzi mwa ana a Davide kuti alamulire zidzukulu za Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Komatu ndidzawamvera chifundo ndi kuwakhazikanso pabwino.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zace kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isake, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweundende wao, ndipo ndidzawacitira cifundo.