Jeremiah 33:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wa Israele, akunenapo mau pa za nyumba za mu mzinda uno ndi za nyumba za mafumu a ku Yuda, zimene anthu adazigwetsa kuti amange zotchinjiriza mzindawo, nthaŵi ya nkhondo. Akuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mudzi uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wa Israeli akunenapo pa za nyumba za mu mzinda muno ndiponso pa za nyumba za mafumu a Yuda. Zidzagwetsedwa, ndipo palibe chifukwa cholimbana ndi mitumbira ya nkhondo ya Ababuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za nyumba za mudzi uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwacinjirizire mitumbira, ndi lupanga: