Jeremiah 33:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ababiloni akubwera kudzauthira nkhondo, ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzaŵapha mokwiya ndi mwachipseramtima. Mzinda umenewu ndaufulatira chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mudzi uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ababuloni akubwera kudzawuthira nkhondo mzindawu ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzawapha mokwiya ndi mwaukali. Ndawufulatira mzinda uno chifukwa cha zoyipa zake zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adza kumenyana ndi Akasidi, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mudzi uno nkhope yanga cifukwa ca zoipa zao zonse.