Jeremiah 33:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda umenewu udzamveketsa mbiri yanga yabwino, ndipo udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemu. Anthu a mitundu yonse pansi pano adzanditamanda ndi kundilemekeza pakumva za zabwino zonse zimene ndauchitira mzinda umenewu. Adzachita mantha ndi kunjenjemera, poona kuti mzindawo ndaupatsa madalitso ndi zokoma zosaŵerengeka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzayesa mudzi uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mzinda wa Yerusalemu udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemerero. Anthu a mitundu yonse adzanditamanda akadzamva za zabwino zonse zimene ndawuchitira mzindawu. Iwo adzachita mantha ndi kunjenjemera poona madalitso ochuluka ndi mtendere zimene ndapereka kwa mzinda umenewu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzayesa mudzi uno cifukwa ca kukondwa, ndi ciyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawacitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira cifukwa ca zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzaucitira.