Jeremiah 34:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inalipo nthaŵi pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi gulu lake lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankaŵalamulira, ndiponso anthu a mitundu yonse, ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira. Nthaŵi imeneyo Chauta adauza Yeremiya kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yake yonse, akuti:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi gulu lake lonse lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankawalamulira ndiponso anthu a mitundu yonse ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yonse yozungulira Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babulo, ndi nkhondo yace yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wace, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yace yonse, akuti: