Jeremiah 34:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulu onse pamodzi ndi anthu wamba, atachita chipangano kuti akapolo aŵamasule, kuti asaŵasungenso mu ukapolo, zimenezi zidachitikadi ndipo adaŵamasula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo akulu onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho akuluakulu pamodzi ndi anthu onse amene anachita pangano ili anagwirizana kuti amasule akapolo awo aamuna ndi aakazi ndi kuti asawasungenso mu ukapolo. Iwo anachitadi zimenezi ndipo anawamasuladi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo akuru onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;