Jeremiah 34:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zaka zisanu ndi ziŵiri zitatha, aliyense mwa inu ammasule mu ukapolo Muhebri aliyense amene adadzigulitsa kwa inu nagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma makolo anu sadandimve ndipo sadasamaleko konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wake amene ali Muhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi chimodzi, mudzammasule akuchokereni; koma makolo anu sanandimvere Ine, sananditchere Ine khutu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wace amene ali Mhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi cimodzi, mudzammasule akucokereni; koma makolo anu sanandimvera Ine, sanandichera Ine khutu,