Jeremiah 34:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe masiku omwe apitaŵa mudatembenuka mtima ndipo nkuyamba kuchita zomwe ndimafuna Ine. Nonse mudamvana zoŵapatsa ufulu Aisraele anzanu. M'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa mudalonjeza kuti mudzachitadi zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kuchita chimene chili cholungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzake; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene itchedwa dzina langa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kucita cimene ciri colungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzace; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene ichedwa dzina langa;