Jeremiah 34:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsono mudasinthanso maganizo, ndipo mwaipitsa dzina langa. Nonsenu mudaŵagwiranso anthu amene mudaaŵamasula aja, nkuŵasandutsanso akapolo anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera m'ukapolo yense kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akachite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu aamuna ndi aakazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera m'ukapolo yense kapolo wace wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akacite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu amuna ndi akazi.