Jeremiah 34:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Simudandimvere, simudalengeze ufulu kuti mumasule abale ndi anansi anu. Chabwino! Ineyo tsono ndidzalengeza ufulu wina kwa inu, ufulu wake wa kufa ndi lupanga, mliri kapena njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu a pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvera Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kuchaola, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova atero: Simunandimvera Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wace, ndi munthu yense kwa mnzace; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kucaola, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.