Jeremiah 34:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simudasamale chipangano chimene mudachita ndi Ine, ndipo simudasunge lonjezo limene mudachita pamaso panga. Tsono Ine ndidzakusandutsani ngati mwanawang'ombe uja amene ankamdula paŵiri napita pakati pa zigawozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanachite mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwanawang'ombe ndi kupita pakati pa mbali zake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu simunasunge pangano limene munachita ndi Ine. Simunasamale lonjezo limene munachita pamaso panga. Choncho ndidzakusandutsani ngati mwana wangʼombe uja amene ankamudula pawiri napita pakati pa zigawozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanacita mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwana wa ng'ombe ndi kupita pakati pa mbali zace;