Jeremiah 34:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pita ukauze Zedekiya mfumu ya ku Yuda kuti Chauta akunena kuti Mzinda uwu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzautentha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova, Mulungu wa Israeli akuti: Pita kwa Zedekiya mfumu ya Yuda ndipo ukamuwuze kuti Yehova akuti mzinda uno ndidzawupereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni ndipo adzawutentha ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova Mulungu wa Israyeli atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo adzautentha ndi moto;