Jeremiah 34:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onsewo ndidzaŵapereka kwa adani ao ndi kwa amene amafuna kuŵapha. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi nyama zakuthengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewa ndidzawapereka kwa adani awo amene akufuna kuwapha. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo za dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za mlengalenga, ndi ca zirombo za pa dziko lapansi.