Jeremiah 34:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzapereka Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi nduna zake, kwa adani ao amene amafuna kuŵapha, ndiye kuti kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni limene nthaŵi ino layamba kubwerera m'mbuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokereani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda ndi nduna zake kwa adani awo amene akufuna kuwapha, kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni limene nthawi ino layamba kubwerera mʼmbuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ace ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babulo, imene yakucokerani.