Jeremiah 34:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidzaŵalamula, ndidzaŵabwezeranso ku mzinda uno. Adzauthira nkhondo ndi kuulanda, ndipo adzautentha. Motero mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa chipululu, mopanda anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, Ine ndidzawalamula, akutero Yehova, ndipo ndidzawabweretsanso ku mzinda uno. Adzathira nkhondo mzindawu, kuwulanda ndi kuwutentha. Ndipo Ine ndidzasandutsa chipululu mizinda ya Yuda kotero kuti palibe amene adzakhalemo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo ku mudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.