Jeremiah 34:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iweyo sudzapulumuka m'manja mwake. Udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka m'manja mwake. Udzamuwona maso ndi maso, ndipo udzalankhula naye pakamwa ndi pakamwa. Tsono adzakutenga kupita nawe ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iweyo sudzapulumuka mʼmanja mwake koma udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka mʼmanja mwake. Udzayiona mfumu ya ku Babuloni maso ndi maso ako ndipo udzayankhula nayo pakamwa ndi pakamwa. Ndipo udzapita ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lace, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lace; ndipo maso ako adzaanana nao a mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babulo.