Jeremiah 34:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma udzafera pa mtendere. Ndipo paja anthu ankafukiza lubani poika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iweyo usanaloŵe ufumu, tsono nawenso podzaika maliro ako adzafukiza lubani. Pokuimbira nyimbo yamaliro azidzati, ‘Ogo nanu! Mbuyathu uja!’ Ndalankhula zimenezi ndine Mwiniwakene,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! pakuti ndanena mau, ati Yehova.