Jeremiah 34:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau a Chauta adamvekanso kwa Yeremiya. Nthaŵiyo nkuti mfumu Zedekiya atapangana nawo anthu onse a ku Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo ao adzaŵamasule.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, mfumu Zedekiya atapangana pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya. Nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Zedekiya atachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo awo adzawamasule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, atapangana Zedekiya pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;