Jeremiah 34:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene anali ndi akapolo Achihebri, aamuna kapena aakazi, aŵamasuledi. Sankayenera kumsunga mu ukapolo Myuda mnzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Muhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzake kapolo wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene anali ndi akapolo a Chihebri, aamuna kapena aakazi awamasule; palibe amene ayenera kusunga mu ukapolo Myuda mnzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Mhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzace kapolo wace;