Jeremiah 35:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adathira nkhondo dziko lino, tidanena kuti, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithaŵe magulu ankhondo a Ababiloni ndi a Asiriya.’ Nchifukwa chake tikukhala kuno ku Yerusalemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu chifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anathira nkhondo dziko lino, ife tinati, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithawe magulu ankhondo a Akasidi ndi Aaramu.’ Kotero ife takhala tikukhala mu Yerusalemu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma panali, pamene Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu cifukwa tiopa nkhondo ya Akasidi, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu.