Jeremiah 35:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akuti, “Pita ukafunse anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko nzeru ndi kumvera mau anga?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga? Ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iyeyu, Yehova Mulungu wa Israeli anawuza Yeremiya kuti: Pita ukawawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko phunziro ndi kumvera mawu anga?’ akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga ati Yehova.