Jeremiah 35:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lamulo la Yonadabu, mwana wa Rekabu, limene adalamula zidzukulu zake kuti asadzamwe vinyo, iwowo asungadi. Samwa vinyo mpaka lero lino chifukwa chomvera lamulo la kholo lao. Ndakhala ndikulankhula nanu kaŵirikaŵiri kukuchenjezani, komabe simudandimvere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ake, asamwe vinyo, alikuchitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Yehonadabu mwana wa Rekabu analamula ana ake kuti asamwe vinyo ndipo lamulo limeneli alisunga. Mpaka lero lino iwo samwa vinyo, chifukwa akumvera lamulo la kholo lawo. Koma Ine ndakhala ndikuyankhula nanu kawirikawiri kukuchenjezani, koma inu simunandimvere Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ace, asamwe vinyo, alikucitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine.