Jeremiah 35:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidatuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Aliyense mwa inu asiye ntchito zake zoipa. Konzani makhalidwe anu, ndipo muleke kutsata milungu ina, musamaipembedza. Motero mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu.’ Komabe inu simudalabadeko, simudandimvere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchera khutu lanu, simunandimvera Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kawirikawiri ndakhala ndikutumiza atumiki anga, aneneri, kwa inu. Iwo akhala akukuwuzani kuti, ‘Aliyense wa inu asiye ntchito zake zoyipa ndi kukonza makhalidwe ake; musatsatire milungu ina ndi kumayitumikira. Pamenepo mudzakhala mʼdziko limene ndinakupatsani ndi makolo anu.’ Komabe inu simunasamale zimenezi kapena kundimvera Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yace yoipa, konzani macitidwe anu, musatsate milungu yina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunandichera khutu lanu, simunandimvera Ine.