Jeremiah 35:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndikuti ndidzaŵaononga Ayuda ndi anthu onse okhala ku Yerusalemu, chifukwa chakuti sadandimvere pamene ndidaŵalankhula, sadandiyankhe nditaŵaitana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala m'Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndidzagwetsera pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu masautso onse amene ndinakonza chifukwa sanandimvere. Ndinawayitana koma iwo sanayankhe.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala m'Yerusalemu coipa conseco ndawanenera iwo; cifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandibvomera.