Jeremiah 35:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya adauza Arekabu aja mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Chifukwa chakuti mudamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndipo mudatsata malangizo ake ndi kuchita zonse zimene adakuuzani kuti muchite,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya anawuza banja la Arekabu mawu onse a Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, kuti, “Munamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mwatsatira malangizo ake onse ndi kuchita chilichonse chimene anakulamulani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kucita monga mwa zonse anakuuzani inu;