Jeremiah 35:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pita ku banja la Arekabu, ukaŵaitane anthu akumeneko kuti abwere m'chipinda chimodzi cha Nyumba ya Chauta. Atafika, uŵapatse vinyo kuti amwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pita kunyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'chipinda china, nuwapatse iwo vinyo amwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pita ku banja la Arekabu ndipo ukawayitane kuti abwere mʼchipinda chimodzi cha Nyumba ya Yehova ndipo akafika uwapatse vinyo kuti amwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pita ku nyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'cipinda cina, nuwapatse iwo vinyo amwe.