Jeremiah 35:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidabwera nawo ku nyumba ya Chauta, ku chipinda cha ophunzira a Hanani, mwana wa Igadaliya, munthu womvera Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, pamwamba pa chipinda cha Maseiya, mwana wa Salumu, mlonda wapakhomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, chokhala pambali pa chipinda cha akulu, ndicho chosanjika pa chipinda cha Maaseiya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinabwera nawo ku Nyumba ya Yehova, ku chipinda cha ophunzira a mneneri Hanani mwana wa Igidaliya, munthu wa Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, chimene chinali pamwamba pa chipinda cha Maaseya mwana wa Salumu, mlonda wa pa khomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, cokhala pambali pa cipinda ca akuru, ndico cosanjika pa cipinda ca Maseya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;