Jeremiah 35:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Takhala tikutsata malamulo a kholo lathu Yonadabu, mwana wa Rekabu, ndipo pa moyo wathu wonse sitidamwe vinyo ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu aamuna ndi aakazi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife takhala tikumvera zonse zimene kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula. Ife ngakhale akazi athu kapena ana athu aamuna ndi aakazi sitinamwepo vinyo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu amuna ndi akazi;